Home Page > PEN Malawi: kulimbikitsa kuwerenga ndi kulemba mu ziyankhulo za kuntchito ndi za ubadwiri/zamakolo

PEN MALAWI

KULIMBIKITSA KUWERENGA NDI KULEMBA MU ZIYANKHULO ZA KUNTCHITO NDI ZA UBADWIRI/ZAMAKOLO

Poona kuti boma silikutekeseka ndi nkhani yotukula ndi kulimbikitsa ziyankhulo zamakolo chinthu chomwe chotsatira chake ndi choti anthu akulephera kuphunzira ndi kumva mauthenga maka okhuza zamakono, bungwe la PEN Malawi mogwirizana ndi mamembala ake, aphunzitsi, akatswiri a ziyankhulo, olemba ndi atolankhani lakonza ntchito yokweza Chichewa chomwe ndi chimodzi mwa ziyankhulo zazikulu za mdziko lino. Chichewa chili ngati chiyankhulo cha dziko la Malawi. Mwa anthu zana limodzi (100) anthu makumi asanu ndi limodzi(60) amagwiritsa ntchito Chichewa bwinobwino. Ngakhale zili chonchi mauthenga ambiri amafalitsidwa mu chingelezi.

Kuyambira ku ndondomeko ya maphunziro, Chichewa chakhala chikungosunthidwasunthidwa kuti aliyense aphunzire kenaka nkuti asukulu ali ndi ufulu wosankha kuchiphunzira mkalasi kapena ayi. Okonza za ndondomeko sakugamula mokhazikika za maphunziro a Chichewa. Pa ntchito zake boma lilibe chikonzero chikweza ziyankhulo zambadwa/zamakolo. Choncho ziyankhulo zomwe amagwiritsa ntchito anthu ochepa zitha kufa.

PEN Malawi yalingalira zomasulira zithimethime za nkhani za kusasiyana pa ntchito za abambo ndi amayi (gender), zachilengedwe(environment), kuzipangira chuma (entrepreneurship), kusintha kwa nyengo, HIV ndi Edzi, kulumala, matenda osapatsirana ngati kuthamanga kwa magazi mthupi, matenda a shuga, komanso za mmene zinthu ziyenera kuyendetsedwera ndi zolembedwa zina zothandiza kuwerenga ndi kulemba. Izi zigawidwa mmasukulu ndi mmagulu amene pulojekiti ikufikira/kukhudza. Potero mzika zochuluka zizatha kutenga nawo mbali pa nkhani zikuluzikulu za mdera lawo ndi zammadera akutali. Potero Pen Malawi iperekaa mlozo ndi changu kudziko lonse pa nkhani ya ziyankhulo ndi chitukuko.