Home Page > PEN Zambia:  Kutukula za Kulemba ndi Kulankhula m’mitundu ndi zilankhulo za mu dziko la Zambia pakati pa anyamata ndi atsikana.
PEN Zambia.lowres

Chongwe Secondary school

M’chaka ca 2012, Boma la dziko la Zambia linakhazikitsanso m’mbali la chigawo chamaphuzilo kuti ana achichepele m’masukulu okalowa giladi mpaka kukafikila giladi 4, ana ameneya aziphuzitsidwa muzilakhulo za chiZambia. Zimenezi, zinali pambuyo palendo, kupyola zaka makumi atatu, ana ankaphuzitsidwa mu chiNgelezi chokha-chokha ngakhale m’magiladiwo akusi. Koma ai, akatswili mu za maphuzilo adapeza ndi kukhazikitsa kuti ana achichepele amadziwa musanga, ndikubvetsa kwambili mwachangu akamaphuzila muzilakhulo za makolo awo.

Ngakhale zitelo, bungwe la PEN Zambia lasikha-sikha ndipo lapezapo bvuto pa zimenezi zakuphuzitsa ana achichepele muzilakhulo za makolo awo, bvuto kweni-kweni nkukhala aziphunzitsi azilakhulozi naonso alibe ukatswili wakulakhula zilakhulozi modziwa bwino ndi mwaluso. Koma ai, bungwe la PEN Zambia lizayesa-yesanso kusewenza kwambili motukula ndinso kuponyapo chidwi paza kuphunzitsana kalembedwe ka nthano ndi ndakatulo mutubungwe twa PEN m’masukulu pakati pa anyamata ndi atsikana azaka 12 kufika 21.

Bungwe la PEN Zambia lidzayesanso kuchita mokumbutsana ndi aziphuzitsi azilakhulozi za mitundu achiZambia, njila, luso ndi kayendetsedwe katsopano poika pamodzi timabungwe tophuzitsana kalembedwe, kuwelenga ndinso pakumalakhula zilakhulozi mosamala ndi mwaluso m’timabungwe pakati pa anyamata ndi atsikana. Ndiponso ndalama zitaoneka, bungwe la PEN Zambia likhoza kujambula bwino ndithu zothandizila kuphuzitsa zilankhulozi za chiZambia, ndinso kuthandiza kuzisanduliza zolembedwazo muzilakhulo za m’dzikoli, kaya zimenezi nkukhala za m’dzikoli kapena za kumaiko ena.

Chifukwa ca timabungwe timenetu tophunzitsana paza malembedwe ndi kumalakhula m’zilakhulo za makolo athu, bungwe la PEN Zambia lizakwezadi kufunikila kwa nzika za dzikoli kupezapo ubwino paza ku masewezetsa zilakhulo zathu. Nchito yotelei paza malembedwe ndi ubwino wa zilakhulo zathuzi likhoza kupatsa chidwi kwambili anyamata ndi atsikana adzikoli kubvetsa ukongola ndi ubwino wa zilakhulozi, ndiye atakopeka ndithu kumalakhula ndi kulemba bwino m’zilakhulozi za makolo athu.